Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 36
Miyambi ya Patsokwe
Chikondi chili m’manja.
-Mawuwa amanenedwa pofuna kuonetsa kuti umafunitsitsa
utakumana ndi mnzako n’kumupatsa moni.
Chikondi ndi kutherana zakukhosi.
-Chizindikiro cha chikondi chenicheni ndi kuululirana zaku-
khosi, osati kusungirana chakukhosi.
Chikumbumtima chinapha njovu.
-Tikachita choipa chikumbumtima, chomwe ndi munthu
wam’kati, chimatiimba mlandu ndipo timasowa mtendere.
Chikumbumtima chikhoza kumakupwetekabe ngakhale utafun-
da mabulangete ambirimbiri. Ndi bwino kumavomereza tikala-
kwitsa ndi kupempha kuti atikhululukire. Nkhani yake imati,
tsiku lina njovu inatenga katundu wa mwini wake. Ndiye kalulu
ataifunsa inakana kuti sinatenge. Kenako kalulu anauza njovuyo
kuti, “Ngati mwatengadi ndi inuyo n’kumakana, chikumbumti-
ma chikuphani.” Njovu inayamba kuchita mantha kwambiri
chifukwa inkaganiza kuti chikumbumtima ndi nyama ina yai-
kulu kwambiri kuposa iyoyo. Njovuyo inasiya kutuluka panja
kuti ikasake zakudya mpaka inaonda kwambiri. Inkaopa kuti
ikumana ndi chikumbumtima. Kenako njovuyo inafa ndi njala.
Phunziro lake ndi lakuti ndi bwino kumavomera ukalakwitsa,
chifukwa ukapanda kutero umavutika ndi chikumbumtima.
Chikumbutsa nkhwangwa n’chikuni.
-Ngakhale tiiwale kanthu kena kapena kuchita mphwayi
kugwira ntchito inayake, tsiku lina pamadzakhala china chotik-
umbutsa chomwe tinaiwala. Nthawi zina mavuto amatichititsa
kugwira ntchito molimbika komanso kugwira ntchito zomwe
tinkaziona ngati zopanda pake.
Chikumbutsa nkhwangwa n’chisanu.
-Ngakhale tiiwale kanthu kena kapena kuchita mphwayi
35