Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 35
Miyambi ya Patsokwe
Chikakuluma chakuda umaopa ndi khala lomwe.
-Munthu wina akakupusitsa, sukhulupirira aliyense.
Chikaona mnzako osamaseka.
-Mnzako akaona tsoka usamamuseke chifukwa mwina mawa
udzaonanso zomwezo.
Chikaonda chimakoma ndi mchere.
-Chinthu chingakhale choipa maka, koma powonjezera tina n’ti-
na tokometsera, chinthucho chimakhalanso chokongola.
Chimodzimodzi mkazi amaoneka bwino ndi kuvala.
Chikaonekera ng’amba, mawa chituluka.
-Mbewu ikamamera imayamba yatukula dothi kenako n’kuon-
ekera. Zinthu zina zikamaoneka pamakhala pataoneka kale
zizindikiro zake.
Chikomekome cha mkuyu, m’kati muli nyerere.
-Osamatengeka ndi maonekedwe a munthu chifukwa nthawi zi-
na mumtima mumakhala moipa. Nthawi zambiri anthu okongo-
la ndi amene amakhala a makhalidwe oipa.
Chikondi cha “chotsa phazi mpondepo.”
-Chimenechi ndi chikondi chenicheni chochitira zinthu limodzi.
Chikondi cha bulangete chopitira limodzi kumanda.
-Chikondi chopanda chinyengo komanso dyera, chokhalira
limodzi pamavuto ndi pamtendere pomwe.
Chikondi cha chotsa phazi m’pondepo.
-Chikondi chodalirika kapena chokondana kuchokera pansi pa
mtima.
Chikondi cha mphaka, chobisa zala m’thumba.
-Chikondi chobisilana cholinga chako chenicheni. Chikondi
chachinyengo.
34