Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 34

Miyambi ya Patsokwe mitondoyo anapukusa mutu posonyeza kuti sanamuone. Ndiyeno alenjewo atachoka, munthuyo anauza Gondwa uja kuti, “Alenje ajatu apita, ukhoza kutuluka tsopano!” Koma gondwayo anayankha kuti, “Tadikirani kaye pang’ono, muli ke- nakake kokoma muno!” Chifundo chidaumitsa mvunguti. -Tiyenera kuona muyeso woyenera pochitira ena chifundo. Ukachitira ena chifundo mopitirira muyeso, ukhoza kuwononga ntchito ngakhalenso moyo wako umene. Chifundo chili m’manja. -Mawuwa amanenedwa pofuna kuonetsa kuti umafunitsitsa utakumana ndi mnzako n’kumupatsa moni. Chifundo chimaitana chifundo. -Munthu ukamachitira ena chifundo, tsiku lina nawonso amadzakuchitira chifundo. Chiimba chili m’mimba. -Kudya n’kumene kumathandiza munthu kuti agwire ntchito. Chikachita mang’a chileke, mawa chituluka. -Munthu akamakana kuti sanalakwe, kungomusiya, tsiku lina choipa chake chidzamutsata ndipo zoipa zake zidzaululika. Chikadzakula, sichidzasowa. -Mawuwa amanenedwa potanthauza kuti khalidwe loipa lika- dzafika poipa, sipadzakhala wodabwa. Chikaipa usataye. -Ngati chinthu chikuoneka chopanda ntchito, usachitaye chifu- kwa tsiku lina chikhoza kudzakhala chofunika. Chikakhala pamuvi sichipheka. -Mawuwa amanena za munthu amene akulephera kugamula mlandu chifukwa choti ndi wa m’bale wake. 33