Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 33
Miyambi ya Patsokwe
akhoza kuoneka ngati sakuganiza chilichonse koma akuganiza
zambiri. Munthu aliyense amadziwa yekha zinthu zimene an-
gakhutire nazo.
Chidziwe n’chipande powomola.
-Aliyense amakolola malinga ndi khama lake. Munthu akady-
eratu kapena akamachita ulesi, amalandira zochepa.
Chifuko sakumbira.
-Chibale chenicheni sichisowa.
Chifulumizo chokoma ukalasa.
-Tiziganiza mofatsa tisanayankhe chifukwa tikhoza kuyankhula
zopanda pake. Komanso munthu umakamba mosangalala
ukamachita zinthu zabwino.
Chifundo chidaphetsa msemamitondo.
-Chifundo nthawi zina chimapweteketsa. Nkhani yake imati,
nthawi ina alenje anavumbulutsa gondwa ndipo anayamba ku-
muthamangitsa. Alenjewo anamupezeketsa gondwayo moti
anangotsala pang’ono kumugwira. Gondwayo anayesetsa kuko-
ka phazi koma sizinam’thandize moti anaganiza zopempha
thandizo kwa munthu wina yemwe ankasema mitondo m’nk-
halangomo. Atatoperatu, gondwayo anapempha wosema mi-
tondoyo kuti, “Ndithandizeni chonde ndagwira mwendo wanu.
Alenjewa akufuna moyo wanga, chonde ndipulumutseni!”
Wosema mitondoyo anamva chisoni kwambiri ndipo anauza
Gondwayo kuti amubisa. Koma popeza panalibe malo pafupi
pomwe akanamubisapo, wosema mitondoyo anangoganiza
zomubisa m’kamwa. Alenjewo atafika anafunsa wosema mi-
tondoyo kuti, “Mwaona Gondwa atadutsa apa?” Koma wosema
32