Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 32
Miyambi ya Patsokwe
wapulumuka pa vuto mwamwayi, si bwino kubwereza ku-
chitanso zomwezo.
Chidakwa chinakana kulipira ngongole ya thobwa.
-Si bwino kumangonamizira anthu amene tikuwaona kuti ndi
zitsiru kapena opepera.
Chidamlendo mbombo.
-Munthu woti akakhala ndi chakudya sakonda kugawira anthu
ena.
Chidebe chopanda kanthu n’chimene chimasokosa kwambiri.
-Anthu opanda nzeru ndi amene amakhala olongolola kwambi-
ri.
Chidede kukanika chitayang’anana.
-Ndi bwino kumayesetsa kuchita khama pochita zinthu. Zichite
kukanika zokha.
Chidule chimapondetsa matope.
-Zinthu zochitika mofulumira kapena mwachidule sizichitika
bwino.
Chidule chinagwetsa njati m’mbuna.
-Si bwino kuthamangira kapena kuchita zinthu usakudziwa
ndondomeko kapena dongosolo lake chifukwa zimenezo zikho-
za kukubweretsera mavuto.
Chibwana cha nyani chokhalira msampha mtengo nawuona.
-Chibwana chachikulu chomwe chikoza kukutsayitsa zambiri.
Chidwi chinapha mkonzi.
-Ukakhala munthu wachidwi ndi wofuna kudziwa chilichonse,
tsiku lina umadzakhala mboni pa mlandu woopsa, mwina
ukhozanso kupeza nazo mavuto.
Chidziwa mwini m’khuto wa fulu.
-N’kovuta kudziwa zomwe munthu akuganiza mumtima. Ena
31