Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 31
Miyambi ya Patsokwe
zimawalowetsa m’mavuto.
Chibwana ndi chironda.
-Mwana sachedwa kuvulala chifukwa alibe mantha. Ndiye mun-
thu wachibwana, kapena wosalemekeza akuluakulu amapeza
mavuto.
Chibwenzi cha bulangete chopitira limodzi kumanda.
-Umenewu ndi ubwenzi weniweni, wopanda chinyengo.
Chibwenzi cha mphaka chobisa zala m’thumba.
-Pali anthu ena omwe amaoneka ngati abwenzi pamaso koma
kumbali amakuganizira zoipa.
Chibwenzi cha nkhwangwa chikoma pokwera.
-Pali anthu ena omwe amakonda anzawo akaona kuti akhoza
kuwathandiza, akangopeza zimene amafuna ubwenzi umathera
pomwepo.
Chibwenzi cha nkhwangwa chokoma pokwera, potsika achita
kuponya.
-Munthu akamakwera mumtengo amanyamula bwinobwino
nkhwangwa koma akamatsika amangoiponya. Mawuwa
amanenedwa munthu akamanyoza anzake chifukwa choti
zimene umafuna zatheka. Munthu ameneyo amamuti wachita,
“chibwenzi cha nkhwangwa chokoma pokwera.”
Chibwenzi n’kuwonjezera.
-Kupatsana mphatso n’kumene kumalimbitsa ubwenzi.
Chibwenzi sichipherana makoswe.
-Ubwenzi weniweni ulibe chinyengo. Chomwe wamuuza
kapena wam’lonjeza mnzako chimakhala chomwecho.
Chibwereza chidaphetsa kunda.
-Munthu ukamachita chinthu choipa n’kupulumuka, tsiku lina
ukamadzati uchitenso anthu amadzakugwira. Ngati munthu
30