Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 283
Miyambi ya Patsokwe
“Zikubwerera” anafa ndi linthumbu.
-Ukamachitira anzako zoipa, zomwezo zimadzakuchitikira
iweyo.
“Zili konku,” kudya kwa Awiza.
-Mawuwa amanena kuti tizidya mofanana ngakhale ndisa-
chitepo kanthu.
“Zili kwa amchira,” gondwa ali m’mphako.
-Mawuwa amanenedwa pokhana kukhudzidwa ndi zinthu
kapena nkhani za ena.
“Zili uko” adabwera chaje osatenga nsomba.
-Tisamatengeke ndi zinthu zongomva koma tizifunsa kuti tidzi-
we chochita. Ngati munthu wina anaona nsomba osafunsa
n’kupezeka wabwera chimanjamanja.
“Zili uku” anathyoletsa mwendo.
-Munthu wina anathyoka mwendo pothamangira zongomva
chabe. Tidziyamba tafunsa kuti tidziwe mmene zilili osaman-
gomvera zilizonse zomwe ena akunena.
“Ziliko” n’kulinga utatosako.
-Ndi bwino kukhala ndi umboni weniweni pa zimene tamva ti-
sanayambe kuchita zinthu.
“Ziri bwino momwemu,” anakhalitsa tsindwi pakhudu.
-Pakhudu ndi pambali. Munthu wina anzake ankamuthandiza
kuika denga pankhokwe yake. Ndiye anangoyankha mopupu-
luma kuti ziri bwino momwemu ndipo denga lidakhala pamba-
li. Anthu ena samaika mtima wawo pantchito, choncho amachita
zosalongosoka ntchitoyo n’kuwonongeka. Ena akabwera
amachita kudzayambiranso poyambirira.
282