Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 282

Miyambi ya Patsokwe “Timwenji ife,” dzungu n’gonera kumodzi. -Munthu angayankhule mawu amenewa podandaula kuti alibe anzake omwe angamamuuze nkhani za pamudzi. “Tidzaona mawa” anagoneka munda. -Si bwino kumachita zinthu mozengereza. Ndi bwino kumachita zinthu pa nthawi yake ngati tikufuna zitiyendere. “Tiyenitiyeni” sachoka, achoka ndi vundumu. -Kungonena mawu okha sikupindula koma kuchita. “Tizimve,” mwana wakwathu ali komweko. -Ngakhale akufuna kubisa tidzamvabe chifukwa anthu amene ali kumeneko ndimadziwana nawo. “Ukaphaneni” suchedwa kulekanitsa mabwenzi. -Ngati anthu ogwirizana amamvera kwambiri zonena za anthu, ubwenzi wawo umasokonekera. “Ukutisokosera” n’kulinga utamva. -Tisamadalire zonse zomwe anthu akutiuza. “Usakanene” ndiye adanena. -Osamakhulupirira anthu chifukwa sasunga chinsinsi. Ukauza munthu kuti asunge pakamwa mpamene amaulula. “Vinavina” savinika. -Si bwino kumakakamiza ena kuchita zimene sakufuna. “Wandiona bwanji?” palibe mlandu wa maso. -Chilichonse chinapangidwa kuti chigwire ntchito yake pa nthawi yakenso. “Zidzalezidzale” adalinda chiswe. -Poyembekezera kuti dengu lidzadze, chiswe chinadya dengulo. Tizichita zinthu mwachangu popewa zinthu zimene zingatileph- eretse. 281