Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 281

Miyambi ya Patsokwe “Pepani” sathetsa mlandu. -Kupepesa ukalakwa kapena ukawononga chinthu chamwini sikukonza zinthu koma kuchitapo kanthu monga kubweza zimene zaonongekazo. “Pita uko” si kuyenda, kuyenda ndi “tiye kuno.” -Ukamaphunzitsa ena ntchito kapena zinazake, si bwino ku- mangowauza zochita. Ndi bwino kuwawonetsa m’mene an- gachitire zinthuzo. “Pwafu” salima, amalima ndi “bwete.” -Munthu amene ali ndi njala sangalime, koma amene wadya. Kuti munthu agwire bwino ntchito, adye kaye. “Pwatapwata phulu,” sapsetsa ndiwo. -Kuti ndiwo monga nyemba zipse, pamafunika ziwire kwa nthawi yaitali. Choncho, kuziphula sikungapangitse kuti zipse. Pochita zinthu umafunika kuzichita motsimikiza mpaka zitatha. “Sokanisokani,” anatenga jekete lothina. -Munthu wina anakasiya jekete lake kwa atelala kuti alibweze. Ndiye ankakakamiza telalayo kuti alisoke mwachangu. Pamapeto pake telala anasoka mwaphuma n’kupezeka kuti iyeyo ataliyesa linali lothina. Kupupuluma si kwabwino. Ndi bwino ena akamatichitira zinthu tiziwapatsa nthawi yokwanira kuti aichite molongosoka. “Tidzaona mawa,” adagoneka munda. -Ndi bwino kuyambiratu kuchita zinthu m’malo modikira mawa, chifukwa zamawa sizidziwika. “Tilawetilawe” anatha lichero la mapira osaviika. -Chizolowezi chimayamba pang’onopang’ono n’kufika poipa. 280