Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 280
Miyambi ya Patsokwe
“Pangapanga” sapangika.
-Kungonena kapena kukalipira anthu sikutanthauza kuti ntchito
ichitika. Pogwira ntchito pamafunika kukambirana komanso
kuthandizana.
“Pano mpakwathu” adagona ndi njala.
-Osamadalira ena kuti atipatsa zimene tikufuna chifukwa
mwina sangatipatse ndiye tingavutike.
“Pano mpathu” n’kulinga utakhuta.
-Kuti munthu usangalale kapena uzichita zina momasuka uma-
funika kudya kaye mokwanira. Koma kuti chakudyacho
chipezeke umafunika kugwira ntchito. Munthu amamera mizu
pamalo ngati pali chakudya chokwanira.
“Pano ndi panga” adakazinga chimera.
-Osamadalira ena kuti atipatsa zimene tikufuna chifukwa
mwina sangatipatse ndiye tingavutike.
“Patse” samatula chiluli, amatula chiluli ndi “taona apa.”
-Munthu wopempha amatha kugwiritsa ntchito zimene wap-
atsidwa mwanzeru pomwe munthu wakuba amangogwiritsa
ntchito zimene wapezazo mosasamala.
“Patsepatse” n’kulanda, munthu woolowamanja amadziwa
yekha.
-Ngati munthu safuna kupereka asanapemphedwe, amaonedwa
kuti ndi womana. Ena ukawapempha amangoperekera manyazi.
Mwambiwu umatanthauza kuti munthu azipereka mwa kufuna
kwake osati kuchita kumukakamiza.
“Pepani” sapoletsa chilonda.
-Kupepesa ukalakwa kapena ukawononga chinthu chamwini
sikukonza zinthu, koma kuchitapo kanthu monga kubweza
zimene zawonongekazo.
279