Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 279
Miyambi ya Patsokwe
“Ndikupha mawa” sali patali.
-Ena akatiuza kuti tidikire, tisamanyinyirike chifukwa nthawi
sichedwa kutha. Chachikulu n’kudikira kuti winayo akwaniritse
lonjezo lake.
“Ndili ndekha ndili ndekha” ndi amene akutha anthu.
-Anthu omwe alibe ana ndi amene amachitira ana a ena nkhan-
za. Ena omwe alibe katundu amabera anthu ena.
“Ndimam’khulupirira” anam’goneka pabwalo.
-Pochita zinthu si bwino kumadalira ena kuti adzatithandiza.
Munthu wina ankayembekezera kuti mnzake akumudziwa
ndipo amupatsa malo ogona. Zitalephereka anagona panja.
“Ndimo alili” n’kulinga utamuona.
-Kuti udziwe khaliwe la wina umayenera kukhala naye, m’malo
mongogamula kuti ndi woipa.
“Ndipatendipate” anapata bala.
-Ukamapupuluma kuti upeze zinazake umakumana ndi
mavuto.
“Nyemba zowola udya chaka chino” n’kulinga uli nazo.
-Munthu sadandaula akawaputa yekha mavuto.
“Nyemereko” adataya nsima kudzenje.
-Pali anthu ena omwe amafuna zonse zikhale zawo moti sasan-
galala ena akapeza zawo. Munthu womana amatha kuwononga
zinthu n’cholinga choti asapatse ena. Mwachitsanzo, pobisa
kupezeka kuti zawonongeka.
“Pali chikomere” adasiya chikho pabwalo.
-Munthu akamaumirira kuchita zoipa amadzasiya chikho
pakhonde, amamwalira n’kusiya zomwe ankakondazo.
278