Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 278
Miyambi ya Patsokwe
tsiku lina.
“Ndidyeretu” adasowa mbewu.
-Tisamatsiriziretu katundu kapena mbewu zonse. Tizisunga zina
kuti zidzatithandize m’tsogolo.
“Ndifa, ndifa” adalaula moyo nthawi yaitali.
-Tisamapange malonjezo opanda pake.
“Ndikanakhala ine” anathawitsa anyani a mwini wake.
-Mawuwa amanena za munthu womva zayekha, wopereka
malangizo osathandiza kapena wosowetsa anzake mtendere.
“Ndikanakhala ine” sapita kumilandu.
-Pali anthu ena omwe amati zinthu zikadutsa amayamba kunena
maganizo awo koma pamene zimachitika anangoti du. Kuchita
zimenezi sikuthandiza.
“Ndikhale nawo” analanda malo.
-Alendo ena amakhala ndi cholinga cholanda malo, moti muka-
panda kusamala amapezeka kuti ayamba kukulamulirani.
Chitsanzo ndi bonongwe. Amayamba ndi m’modzi koma ke-
nako amadzadza munda wonse.
“Ndikometsendikometse” ndiko kuipitsa.
-Osamachita zinthu chifukwa chongofuna kuyamikiridwa,
mapeto ake umalakwitsa kapena kuwononga zinthu.
“Ndikonzendikonze” adanyula mtembo wa eni.
-Si bwino kumachita phuma pa zinthu chifukwa umatha kupal-
amula nazo.
“Ndikudziwa kale” adamanga nyumba yopanda khomo.
-Munthu amene amadziyesa wodziwa zonse amalephera kufun-
sa ena, mapeto ake amalakwitsa anthu n’kumuseka. Ndi bwino
kumafunsa ena.
277