Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 277
Miyambi ya Patsokwe
“Ndakhupuka” adagwetsa nyumba.
-Si bwino kumadzitama ndi zimene tili nazo chifukwa sitidziwa
za mawa.
“Ndakulapa” n’kulinga utayenda naye.
-Kuti munthu udziwa khaliwe la mnzako umayenera kukhala
naye pafupi osati kungomuona.
“Ndakuona” adalasa galu.
-Munthu wina ali kosaka nyama anzake anamufunsa ngati waio-
na nyama. Iye anangovomera chifukwa ankaona kuti achita
manyazi ndipo anagenda n’kupha galu wake yemwe. Ngati
sukudziwa zinazake si bwino kungovomerera manyazi. Ndi
bwino kupempha ena kuti atithandize.
“Ndakwatira” n’kulinga utagonera.
-Osamafulumira kunena kuti wapeza banja labwino mpaka
patatha nthawi ndithu, chifukwa anthu ena amabisa khalidwe
lawo poyamba.
“Ndaonera momwemo,” mwambi wa gulugufe.
-Tsiku lina gulugufe ankamwa timadzi ta m’maluwa. Ena pomu-
funsa anati: “Kodi ukhuta timadzi tomweto?” Gulugufeyo
anayankha kuti, “Ndaonera momwemo” kutanthauza kuti nda-
vomera zonse zimene mukunenazo. Mawuwa amatanthauza
kuti tizikhutitsidwa ndi zimene tili nazo ngakhale ena atama-
khamba kuti sangathe kukhala moyo wachoncho.
“Ndapakonda” adasiya khonde.
-Ukakhala mlendo uyenera kudziwa nthawi yochoka chifukwa
ukakhalitsa eni ake amatopa nawe ndipo amasiya kukusamalira
ngati mlendo.
“Ndichite bwino,” gondwa anafa.
-Munthu wochita zinthu modzitama, amadzachita manyazi
276