Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 276
Miyambi ya Patsokwe
“N’chomwecho” chidaletsa Nkhandwe kubwera kumudzi.
-Nkhandwe imakonda moyo wakutchire. Munthu azichita zin-
thu zimene zimamukomera.
“N’dzalemera” adamka ndi nguwo ya insa.
-Osamazengereza kugwira ntchito chifukwa ukakhala waulesi
umangosaukirasaukirabe mpaka kufika povala chikopa cha insa.
“N’konzen’konze” adanyula maliro a eni.
-Munthu usamajijirike pa zinthu za eni chifukwa ukhoza kupeza
mavuto ngati utalakwitsa chinachake.
“N’konzen’konze” adasupula mtembo wa eni.
-Si bwino kumachita phuma pa zinthu chifukwa umatha kupal-
amula nazo.
“N’kulen’kule” adagwa padzala.
-Kuthamangira kudziwika kumagwetsera munthu m’mavuto.
“N’kulendinen’kulendine” adagwa padzala.
-Munthu wodzikuza komanso wonyada, anthu ena ama-
muchepetsa n’kumuchititsa manyazi.
“N’tapen’tape” adataya lipande.
-Timafunika kuchita zinthu mwachifatse, osapupuluma chifu-
kwa ukapululuma umawononga zinthu ngati munthu amene
akufuna kuchotsa lipande (mphale) mumtondo n’kumachita
mwachangu kwambiri amataya mphale yambiri.
“Ndafulumira” adadya zosapsa.
-Tisamachite zinthu mofulumira kwambiri chifukwa pamapeto
pake zimakhala zosalongosoka. Tisamafotokoze nkhani yomwe
sitinaimvetse bwino, chifukwa tingafotokoze zosapsa.
“Ndafulumira” anasiya tonde m’khola.
-Changu nthawi zina chimawononga zinthu monga munthu
amene sanatsegulire ziweto zake.
275