Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 275
Miyambi ya Patsokwe
pomwepo.
“Kwazizira” alibe mpani.
-Munthu waulesi amakhalanso ndi njala. Tiyenera kugwira
ntchito kuti tipeze zimene tikufuna.
“Mbewa zidyana,” amatero Aphiri pofunsira Naphiri.
-Mawuwa amanenedwa ngati anthu a pachibale akuchita zosay-
enera pophwanya chikhalidwe chawo monga pankhani ya kuk-
watira.
“Mchakwawo” adanka ndi madzi.
-Tisamalekerere anthu akuchita zoipa kapenanso akusochera
pongoganiza kuti adziwa chochita popeza ndi aakulu msinkhu
kapena ophunzira kwambiri. Mpofunika kuwachenjeza ndi ku-
wathandiza kuti asagwere m’mavuto.
“Momwemo” walinga utamwamo.
-Kuti munthu udziwe zinthu, umayenera kuzichita kaye.
“Mpokoma pano” ndiye kuti mwagona awiri.
-Kuti munthu uyamikire kuti pamudzi kapena pakhomo ndi
pabwino, umayenera kucheza ndi ena n’kumva za anthu a
pakhomopo.
“Mulungu akundiona” anadyedwa ndi ng’ona.
-Mulungu amathandiza munthu yemwe amadzithandiza yekha.
“Muonere ine” adadyedwa ndi ng’ona.
-Si bwino kumadzionetsera kuti timadziwa zinazake, chifukwa
tikhoza kupeza mavuto.
“Mwana wa a uje wasamba” n’kulinga atakhuta.
-Ngati mwana wasamba m’manja atadya ndiye kuti wasangalala
ndipo wakhuta. Tizipatsa ana zinthu zokwanira kuti azisangala-
la.
274