Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 274
Miyambi ya Patsokwe
kumusangalatsa komanso kumulangiza. Pawekha sungachite
kalikonse.
“Ili kutali mvula,” m’mera uona ng’amba.
-Mawuwa amagwiritsidwa ntchito pamlandu ngati mboni
yachedwa. Mboniyo ikachedwa, mlandu umayambikabe. Aka-
bwera, adzapereka umboniwo panthawi yake. Mwambiwu
umalimbikitsa anthu kuti azichita zinthu pa nthawi yake.
“Ili kutali mvula,” mpesa umera m’ngamba.
-Zinthu zimachitika panthawi yake mosatengera kuti wina
kapena chinachake palibe.
“Ine panalibe” adang’amba thumba.
-Kumvetsera ena akamakufotokozera zimene zinachitika iwe
kulibe n’kothandiza kuti usanene kapena kuchita zinthu zomwe
sumayenera kuchita.
“Izo zokha ndiye ayi,” fisi adakana nsatsi.
-Si zonse zimene anthu amanenera munthu zimakhala zoona.
Ngakhale munthu atakhala wamakhalidwe oipa, pamafunika
umboni weniweni tisanamunene kuti wachita cholakwa.
“Kakadachepa,” n’kuona msandulizo.
-Tizipempha thandizo kuchoka kwa anzathu zinthu zisanafike
poipa.
“Kwapita apongozi,” n’kulinga utawaona.
-Umayankhula za chinthu chimene wachiona kapena ukuchidzi-
wa.
“Kwaya kwaya” ndi uchitsiru, wochifuna apempha yekha.
-Osamakakamiza munthu kuchita zimene sakufuna.
“Kwaya kwaya” wam’kamwa, mtima uli pomwepo.
-Mawuwa amanena za munthu amene amalonjeza kukupatsa
chinthu asakufuna kukupatsa kapena mtima wakenso uli
273