Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 273
Miyambi ya Patsokwe
“Gona n’kuphe” sali patali!
-Ena akatiuza kuti tidikire, tisamanyinyirike chifukwa nthawi
sichedwa kutha. Chachikulu n’kudikira kuti winayo akwaniritse
lonjezo lake.
“Gona” ndi mwini nyumba (mudzi).
-Ukakhala mlendo sungachite kapena kutenga kalikonse,
pokhapokha eni pakhomopo atakuuza.
“Gona” ndi mwini wake wa nyumba.
-Ulamuliro wa chinthu umayenera kuchoka kwa mwini wake
chinthucho.
“Ichi chakoma, ichi chakoma,” pusi adagwa chagada.
-Osamangotengeka ndi chilichonse koma kumaika mtima pa-
chinthu chomwe ukufuna. Ukamati uku wapita, uku wapita,
mapeto ake umalephera zonse.
“Ichi chakoma,” adagona m’khufi atafika kwawo.
-Ukamakonda kwambiri zosangalatsa, umayenera kudziwa kuti
mavuto akukusunzumira mochenjera.
“Ichi n’changa” chidapinditsa mchira wa nyani.
-Nthawi zina chifukwa cha umbombo timawonongetsa zinthu.
Munthu angaganize kuti, “Ndikatulutsa pano ndidya ndi
anzangawa,” akamati akaone amakapeza zawonongeka.
“Ichi n’changa” chinaolera pansalu.
-Kuumira kumachititsa kuti zinthu ziwonongeke.
“Ichi n’chiyani” n’kulinga muli awiri.
-Anthu akakhala awiri amatha kuchita zinthu modalirana ndipo
amatha kuthandizana wina akapeza mavuto.
“Ichi n’chiyani” n’kulinga muli awiri.
-Munthu aliyense amafuna wina woti azimuphunzitsa,
272