Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 272
Miyambi ya Patsokwe
Ya M’mitengero
“Akuchita dala” adapita ndi madzi.
-Tisamalekerere anthu akuchita zoipa kapenanso akusochera
pongoganiza kuti adziwa chochita popeza ndi aakulu msinkhu
kapena ophunzira kwambiri. Mpofunika kuwachenjeza ndi ku-
wathandiza kuti asagwere m’mavuto.
“Andilekere” adapha make.
-Kuti zinthu zitiyendere bwino, tizipempha mnzeru kwa ena,
apo ayi tikhoza kuchita zinthu zomwe tinganong’oneze nazo
bondo.
“Bongololo ndi ndiwo” uli ndi anzako amene umadya nawo.
-Umboni umafunika ngati ukuchita zinthu kuti udziwe ngati
ukulondoladi.
“Chitachita” sachichitika.
-Kuumiriza kapena kuzunza anthu pogwira ntchito sikuthandi-
za, chifukwa mapeto ake ntchitoyo ndi imene imawonongeka.
“Chitani” adagulira nkhwangwa matowo.
-Pafunika kuganizira mofatsa tisanagule chinthu chifukwa
mwina tikhoza kungowononga ndalama pachinthu chopanda
ntchito kwenikweni.
“Chitani” adakafera kunyanja.
-Munthu wolamula asodzi anafera kunyanja chifukwa chosadzi-
wa kupalasa bwato. Nthawi zonse ankangouza ena kuti apalase.
Pofuna kuchita kanthu kena pafunika kufunsa ena kuti atithan-
dize kachitidwe kake, kenaka n’kuganizira bwino ngati tingathe.
Zinthu zoumiriza sizichita bwino.
“Diso la Lumbe lili m’kamwa,” n’kulinga utaliona.
-Sibwino kumanena zinthu zimene sukuzidziwa bwinobwino.
271