Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 270
Miyambi ya Patsokwe
kudzamuona kuti adzamupatse mphatso.
Ziliko n’kulinga utatosako.
-Si bwino kutsimikizira chinthu usadapeze umboni wokwanira.
Umboni weniweni umafunika kuchoka pa zimene waziona.
Zimene wamkulu angaone munthu wamkulu atakhala pansi
zingapose zimene mwana angaone ataimirira.
-Akuluakulu amadziwa zambiri chifukwa akumana ndi zambiri
pamoyo wawo. Ndi bwino kumamvera malangizo awo.
Zina kambu zina leku.
-Umafunika kusankha zoyenera kuyankhula kapena ayi.
Zinapangana zinaulukira pamodzi.
-Tiyenera kumachita zinthu mogwirizana.
Zingale akaipa, aipa ndi nthenga zomwe.
-Munthu woipa mtima amaipa ndi mawu komanso zochita zom-
we. Zochita zakezo zimakhudzanso abale ake.
Zingalume phula nditenga.
-Mawuwa amanenedwa kuti ngakhale akumane ndi mavuto
otani, sasiya mpaka atapeza chimene akufuna.
Zingwinjiri sizipanganika, zimalira m’thumba la mbala.
-Munthu wina ataba zingwinjiri anagwidwa zitalira m’thumba.
Choipa sichingabisike chimaululika.
Zingwinjiri zimalira zikakhala ziwiri.
-Kuti zinthu ziyende timafunika kuthandizana.
Zingwinjiri zimalira ziwiri, osati chimodzi.
-Anthu akakhala awiri amathandizana pa zambiri. Munthu aka-
khala wodzikonda zikamuvuta amasowa womuthandiza.
Zinthu zimayenda ndi zinzake.
-Anthu opeza mofanana amagwirizana.
269