Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 268
Miyambi ya Patsokwe
Zakumva zimapweteketsa mutu.
-Osamangomvera zilizonse chifukwa zina zimakhala zabodza
ndipo zimangokupatsa nkhawa.
Zakusimba saulula.
-Tizisunga chinsinsi, osamangoulula chilichonse chimene tamva
ngati kuti kamwa lathu lili ndi chiboo.
Zala sizifanana, nawoso anthu amasiyina.
-Tiyenera kumachitira aliyense mofanana. Ngakhale kuti zala
ndi zotalika mosiyanasiyana, zonse zimafuna kusamaliridwa
mofanana.
Zam’dengu zimapindula ukachita khama.
-Malonda amafunika khama komanso kulimba mtima.
Zamwini sakulira mwendo.
-Si bwino kumachita matama chifukwa cha zinthu za eni kapena
kumanyoza ena chifukwa cha chuma cha abale athu.
Zamwini savalira thewera.
-Tisamalowerere nkhani za anthu ena.
Zanga zili kuphiri, zifulumira kutsika.
-Tisamakongole tilibe podalira.
Zangazanga zidathyola bwampini msana.
-Munthu amene amangosonkhanitsa zinthu zomwe sangazig-
wiritse ntchito ndi wopusa chifukwa amangovutika.
Zaona atondo n’zolaula.
-Atondo ndi mbewa. Mbewazi zinakumana ndi mavuto aakulu
zitakodwa mumsampha. Aliyense akhoza kukumana ndi
mavuto.
Zathu, salowa m’khola.
-Munthu m’modzi sakhala ndi mphamvu pa zinthu zagulu.
267