Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 267
Miyambi ya Patsokwe
Za eni n’za eni, madzi amoto satentha nyumba.
-Sitiyenera kumajijirikira zinthu za eni chifukwa tikhoza
kungopusapo.
Za kumzinda saulura.
-Ndi bwino kuti tizisunga chinsinsi cha zimene tamva kapena
kuona.
Zabwino zili m’tsogolo.
-Ngati munthu utayesetsa kuchita khama, ukhoza kukhala ndi
tsogolo labwino.
Zachoka ndundu tiyanike inswa.
-Mwambiwu ndi wofanana ndi wakuti, “Achoke malizagudu, ti-
yanike inswa ziume.” Umanenedwa posangalala kuti anthu
amene sumafuna kuti akhalepo ukamachita zinazake achoka.
Zachoka ndundu tiyanikeko inswa.
-Anthu ena omwe safuna kuti anzawo amveko zachinsinsi zawo
amayesetsa kuti akambirane zachinsinsizo ena aja akachokapo
kapena amapita pamalo oduka mphepo.
Zadzera usetekera, mkombaphala anaduka chala.
-Chala chamkombaphala chikhoza kuduka chifukwa chochig-
wiritsa ntchito udyo. Tizichita zinthu moyenera.
Zafera m’mazira.
-Zalephereka, sizinapite patali.
Zakuba sizilemeretsa.
-Munthu amene ali ndi zinthu zakuba sazisamalira ngati mmene
zikanakhalira akanagwira ntchito.
Zakumva zimaondetsa.
-Osamangomvera zilizonse chifukwa zina zimakhala zabodza
ndipo zimangokupatsa nkhawa.
266