Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 264
Miyambi ya Patsokwe
Wotuwa m’pemphe mafuta.
-Osauka nthawi zina amatha kukhala ndi zinthu zimene olemera
alibe, monga masingano.
Wotuwa ndiye amafuna mafuta.
-Ndi munthu amene ali pamavuto amene amayesetsa kuti apeze
zimene akufuna.
Woumba mbiya alibe mkhate.
-Si bwino kumaumira kugwiritsa ntchito zomwe tili nazo.
Woumba mbiya amaphikira m’phale.
-Nthawi zina munthu wogwira ntchito zaluso sakonda
kutengako chimodzi chifukwa choganiza kuti akatero akuwo-
nonga. Iye amagwiritsa ntchito zipangizo zakutha kapena
zosweka.
Woumba mbiya saphikira m’phale.
-Si bwino kumaumira kugwiritsa ntchito zomwe tili nazo.
Woumiriza ndiye amapha nyama.
-Nthawi zina chinthu choumirizidwa ndi chimene chimatheka
komanso kuchitidwa bwino kwambiri.
Wovala nyanda salumpha moto.
-Nyanda ndi kampango komwe azimayi amavala m’chiuno.
Nyanda sichedwa kugwirira moto. Si bwino kumachita zinthu
zimene zingatiike m’mavuto monga kuchita chiwerewere ndi zi-
na.
Wovinidwa sapisa dzanja m’mphika wa ndiwo.
-Tiyenera kusiya kuchita zachibwana tikakula.
Woyenda ndi lupanga amafa ndi lupanga lomwelo.
-Chinthu chimene umakonda n’chimene chimakupha.
263