Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 263
Miyambi ya Patsokwe
Wosoka mphasa amagonera pazidutswa.
-Nthawi zina munthu wogwira ntchito zaluso sakonda
kutengako chimodzi chifukwa choganiza kuti akatero akuwo-
nonga. Iye amagwiritsa ntchito zipangizo zakutha kapena
zosweka. Mwachitsanzo, woluka mphasa akhoza kumagona
pansi, akasoka mphasa kumangogulitsa.
Wosoka mphasa amagona pamachika.
-Nthawi zambiri anthu amene amasoka mphasa ndi amene ama-
gonera mphasa zakutha. Ndi bwino kumasungako zinthu zina
kuti tigwiritse ntchito.
Wosuma chakudya alibe mawu.
-Ngakhale tikusowa zinthu zina, tiyesetse kumakhutitsidwa ndi
zomwe tili nazo.
Wotchera ulimbo satsokomora.
-Pa mlandu timafunika kuyankhula mosamala kuti tisaulule zi-
na.
Wotengera Nguluwe kuutsa n’chayamba kale.
-Anthu amene amavumbulutsa nguluwe kutchire n’kuigwira
amafunika kukhala oti anayamba kale. Ukapeza ena akuchita
zinthu zachilendo si bwino kungoyamba kuchita nawo, mwina
iwowo amadziwa machitidwe ake.
Wothabe upse mbala.
-Ukamayenda ndi anthu oipa, usamadabwe ukagwera
m’mavuto.
Wotsirira anzake amatsiriridwa.
-Ukachitira anzako zabwino nawonso amakuchitira zabwino.
Wotuwa mpake mafuta.
-Tiyenera kuthandiza ena omwe akuvutika.
262