Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 262
Miyambi ya Patsokwe
Wopunduka n’Chauta, mpembedzeni.
-Tiyenera kulemekeza anthu ngakhale atakhala wolumala chifu-
kwa nawonso ndi ana a Mulungu.
Wopupuluma anadzikodzera chifukwa cha mvula yongodutsa.
-Mawuwa anabwera chifukwa cha munthu wina yemwe ankafu-
na kutaya madzi. Ndiye poona kuti mvula ikubwera ndipo
anyowabe, anangodzikodzera koma mvulayo inangolambalala
umo, osamunyowetsa moti anachita manyazi kwambiri. Tisama-
pupulume pochita zinthu.
Wopusa amamanga nyumba, wochenjera nagula.
-Ndi bwino kumaganiza kaye tisanachite chinthu kuopa kuchita
zinthu zopanda mnzeru.
Wopusa anaomba ng’oma, wochenjera navina.
-Nthawi zina anthu amene amaoneka opusa ndi amene anga-
tithandize. Tiziona ena kukhala otiposa pa chinachake.
Wosamva adamva nkhwangwa ili m’mutu.
-Munthu wosamvera malangizo amadzawamvera atakumana
kale ndi mavuto. Kumamva nkhwangwa itafika kale m’mutu
komwe ndi kumva mochedwa.
Wosamva za anzake n’chitsiru.
-Munthu amene samva za anzake amakhala chitsiru, wopulukira
komanso wosadziwa kanthu chifukwa saphunzira chilichonse
kuchokera kwa ena.
Wosamvera za anzake adalira ching’ang’adza.
-Munthu amene ndi wosamvera ena, amadzilirira yekha aka-
kumana ndi mavuto.
Wosauka ndiye wolemera.
-Wosauka ndiye amapeza tulo komanso kusangalala ndi zomwe
wapeza pomwe wolemera sapeza tulo.
261