Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 261

Miyambi ya Patsokwe Wolirira kwawo adapita ndi madzi. -Mawuwa amachenjeza munthu amene akuchita makani anzake akamamulangiza. Anthu ngati amenewa amakhala ngati akudzi- wa zonse ndipo pamapeto pake amakumana ndi mavuto oopsa. Wolondera chitsime safa ndi ludzu. -Munthu amadyera ntchito imene amagwira monga wodikirira chitsime sangasowe madzi. Woluka nsengwa (malichero) adyera m’chipapa. -Nthawi zina munthu wogwira ntchito zaluso sakonda kutengako chimodzi chifukwa choganiza kuti akatero akuwo- nonga. Iye amagwiritsa ntchito zipangizo zakutha kapena zosweka. Wongolozera kumtondo, kumunda kulibe ndime. -Mawuwa amanena kuti tisamakhale aulesi, anthu omangokon- da kudya osati kulima. Wonukha samadzimva, amamumva ndi anzake. -N’zovuta munthu kudziwa kulakwa kwako kapena makhalid- we ako oipa koma anzako. Ndi bwino kumafunsako ena kuti ati- uze mavuto athu. Wopempha salira tololo. -Tizikhutitsidwa ndi zomwe tili nazo kapena tapatsidwa. Mwachitsanzo, munthu wopemphetsa samafuna kuti amupatse zodzadza thumba. Wopemphetsa sakulitsa chitete. -Wopemphetsa amafunika kumakhutira ndi zimene wapatsid- wa. Wophikira ena amafa ndi njala. -Tiziyamba kuona zosowa zathu kaye tisanayambe kuthandiza ena. 260