Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 260
Miyambi ya Patsokwe
wochitanso zina.
Wokaona nyanja anakaona ndi mvuu zomwe.
-Ukayendera zina umatha kukakumananso ndi zina zomwe
sumayembekezera.
Wokoma atani wonga fungwe.
-Mawuwa amanenedwa munthu akamadandaulira anthu osaya-
mika ngakhale utawachitira zabwino.
Wokoma sagonera.
-Anthu abwino sakhala moyo nthawi yaitali.
Wokumba ndi amene amayenda ndi mchopolo.
-Mchopolo ndi ndodo yokumbira. Munthu sangakumbe popan-
da chokumbira. Tiyenera kukonzekera bwino tisanayambe ku-
chita chilichonse.
Wokwatira azidya mapira.
-Pabanja pamakhala mavuto ambiri omwe amafunika kupirira.
Ndiye mapira ndi mbewu imene imapirira chilala. Choncho,
kudya mapira kukutanthauza kuti munthu amene ali pabanja
ayenera kukhala wopirira.
Wolanga mwambo sachita.
-Anthu ena amangodziwa kuuza anzawo zochita koma iwowo
osachita. Kuti malangizo akhale ogwira mtima umafunika
uyambe kaye iweyo kuwatsatira.
Wolemera ndi amene amakhutira ndi zomwe ali nazo.
-Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka bwanji, koma osama-
khutira, munthu woteroyo sangakhale wolemera. Kulemera
kwenikweni n’kukhutira ndi zimene uli nazo.
Wolira samugwira pakamwa.
-Munthu amene akulira mumafunika kumusiya kuti ayankhule
zakukhosi kwake.
259