Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 26
Miyambi ya Patsokwe
Chalimba chalimba, shati sikhala yopanda kolala.
-Ngakhale chinthu chikhale champhamvu, chimasowabe china
chochichirikiza. Aliyense ndi wofunika.
Chalowa m’khutu chayanza malo.
-Chimene munthu wamva sangachitulutsenso. Choncho, mpo-
funika kuchenjera polankhula kuopa kulakwitsa.
Chalowa m’khutu, chalowa.
-Zimene munthu wamva, zimakhala kuti wazimva basi.
Sungachitenso chilichonse kuti zibwerere. Tizisamala ti-
sanayankhule.
Chambo chimaona konse.
-Munthu ukakhala pabanja, si bwino kumathandiza abale ako
okha. Umayenera kumathandizanso abale a mkazi kapena
mwamuna wako.
Chamkuka nkhali yagaga.
-Mawu amenewa amanena za munthu waulesi, wongokonda
kukhala m’nyumba. Chomwe amadziwa ndi kudya basi.
Chamuna sayanika.
-Munthu ukakhala ndi mphamvu usamadzionetsere, chifukwa
tsiku lina umadzakumana ndi anzako omwe amadzakuphu-
vumula n’kukuchititsa manyazi.
Chamwini m’chamwini, ungalimbe maka.
-Anthu ena maso amangokhala pa zinthu za anzawo,
osakhutitsidwa ndi zomwe ali nazo. Tifunika kumachenjera ndi
anthu amenewa. Osamadalira kwambiri zinthu za ena.
Changodza m’chironda, mankhwala palibe.
-Mawuwa amanenedwa munthu akamadandaula kuti, ngakhale
mavuto monga matenda komanso milandu abwera, palibe njira
yowathetsera.
25