Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 259

Miyambi ya Patsokwe kuchinamwali ndi amene amatenga tambala akamapita ku- chinamwaliko. Kukhala bwino ndi anthu n’kothandiza. Wodyera kuyenda adatha mtunda ndi kukhuta. -Munthu amene amangoyendayenda mwa anzake n’ku- mapemphetsa samafa ndi njala. Wofulumira kunena adathawitsa Likongwe la apongozi. -Nkhaniyi imanena za mkamwini wina yemwe anafulumira kunena kuti amene atathawitse Likongwe wa apongozi asamuka pamudzi. Ndiye zinachitika kuti likongwe atabulika anathawira mbali yake ndipo iyeyo anambwita. Basitu, anasamuka pamudzi chifukwa chopupuluma kuyankhula. Tisamatsogoze mawu zin- thu zisanachitike. Wofunsa ndiye afunsa kutali. -Kufunsa zinthu zisanasokonekere n’kothandiza kusiyana ndi kumafunsa zitavuta kale. Wofunsa simung’ambira nguwo. -Kufunsa si kulakwa, choncho wina akatifunsa tisamamupsere mtima, kumung’ambira nsalu yake. Koma tizimuthandiza ndi vuto ali nalolo. Woipa athawa yekha. -Munthu amene wapalamula amathawa popanda womuthaman- gitsa. Mwachitsanzo, akangoona apolisi amaona ngati akufuna iyeyo. Wojeda salipira, alipira ndi woseka. -Kuseka zinthu zopanda pake sikuthandiza. Tisamauze ena nkhani zimene tangomva chifukwa zina zimakhala zabodza. Tingapalamule nazo. Wokaona nyanja adakawona ndi mvuwu zomwe. -Nthawi zina ukamayendera zina umathanso kuchita mwayi 258