Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 258
Miyambi ya Patsokwe
Watuluka m’mphuno n’kulowa m’kamwa.
-Mawuwa amanena za munthu amene sanakwatire kutali,
mwina wakwatira pafupi ndi mudzi wake, kapena wakwatira
msuweni wake.
Wavina kumadzi.
-Mawuwa amanena mokokomeza za munthu amene amatamba
usiku. Kumadzi ndi kumtsinje. Malinga ndi zikhalidwe za ku
Africa kuno, ena amakhulupirira za ufiti ngakhale palibe umbo-
ni wokwanira woti ulipodi.
Wawona Nkhanga maanga wataya Nkhwali.
-Si bwino kutengeka ndi zinthu chifukwa cha maonekedwe.
Ukhoza kupezeka kuti wataya mwayi wopezapeza.
Wayanja mbatata, wataya mpeni.
-Mawuwa amatanthauza kusiya zinthu zenizeni n’kumalimbana
ndi zinthu zosafunika.
Wayenda wapenga, wagona wafa.
-Ngati munthu wapita kuchilendo ayenera kumakumbukira kuti
tsiku lina adzabwerera kwawo.
Wochenjera ndi munthu amene amati akaona tsoka amabisala,
koma chitsiru chimangopitabe n’kukumana ndi mavuto.
-Mwambiwu ndi wochokera m’Baibulo koma anthu ambiri
amaugwiritsa ntchito pochenjeza anthu ena omwe amachitabe
zinthu zomwe akudziwa kuti zikhoza kuwaika m’mavuto.
Wodya nyemba amaiwala, koma wotaya makoko saiwala.
-Zimene anthu ena amachita amaziiwala, koma amene
wachitiridwayo zimavuta kuti aziiwale.
Wodya za kuchinamwali akudza ndi tambala.
-Mawuwa amatanthauza kuti munthu amene amakadya
257