Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 257

Miyambi ya Patsokwe Watenga kafukanyeka. -Kafukanyeka ndi matenda opatsirana. Mawuna amanenedwa ponena za munthu amene watenga matenda osachiritsika chifu- kwa cha chiwerewere. Watenga kamwana, wasiya amawo. -Mawuwa amanedwa ngati munthu wina wapusitsa mnzake. Munthu wopusitsidwayo amanena kuti akuona ngati wachenje- ra atatenga kamwana n’kusiya manthu. Akadzabweranso adzaona. Watenga ya kunkhuni kumchere amwera madzi. -Mawuwa amanena za munthu amene akufulumira kuchita zin- thu ngati mmene amachitira munthu amene ali ndi ludzu loopsa chifukwa choti akuchokera kotola nkhuni. Munthu wotere amatha kumwa madzi amchere chifukwa chopupuluma kuti aphe ludzu lake. Watha m’kamwa muuzimba zikalimo. -Mwambiwu umanenedwa pamene mlandu wagamulidwa ko- ma anthu sakukhutira ndi chigamulo. Nkhaniyo imakhala sinathe atakumana ku uzimba wina akhoza kubaya mnzake ali naye chifukwayo. Wathundukwa, wadya yapaphewa. -Mawuwa amanedwa poloza wina chala kuti ndi mfiti ndipo wadziwika. Watukwana nankungwi mawere atamera. -Mawuwa amanena za munthu amene wachitira mwano aku- luakulu kuiwala zoti awafuna. Mwachitsanzo, wachinyamata kunyoza nankungwi wake atayamba kumera mabere. Tiyenera kumalemekeza akuluakulu chifukwa ndi amene angatithandize. 256