Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 256

Miyambi ya Patsokwe miseche za wina, mwini wake akumva. Waponya katapita. -Kulephera kapena kunena mawu zinthu zitapita. Wapsa phwetekere kumunda kwa make Chenjerani. -Mawuwa amanenedwa pantchito kapena malo ena pochenjeza- na kuti bwana kapena woyang’anira akubwera. Mawuwa amanenedwanso podziwitsa anthu kuti kuyamba gule wamku- lu. Wasekerera fupa wayesa mnofu. -Munthu asamangokhutira ndi zimene akudziwa kapena zimene waphunzira. Akhoza kudabwa atazindikira zinthu zinanso zo- funika kwambiri. Wasosolera pamsampha. -Kumeneku ndi kuchenjeretsa munthu. Angatanthauzenso ku- chita choipa ena ake akuona. Watcha ndikupenya, msampha wakewo uwola. -Pamene munthu wina ankatchera msampha, nkhanga inaona ndipo inachenjera. Mwambiwu umatanthauza kuti munthu akhoza kumva zinazake n’kuchenjera kuti asagwere m’mavuto. Watchera kumwezi, Nkhanga zaona. -Munthu wina ankatchera msampha mwezi ukuwala ndiye nkhanga zinaona n’kuchenjera. Mwambiwu umatanthauza kuti munthu akhoza kumva zinazake n’kuchenjera kuti asagwere m’mavuto. Ukafuna kumugwira munthu si bwino kuulula njira zako. Watchera kumwezi. -Munthu akamachita zachinyengo, nthawi imafika yomwe anzake amamutulukira. 255