Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 255
Miyambi ya Patsokwe
Wanga ndi wamalonda.
-Munthu woumira safuna kungopereka zinthu mwaulere.
Wangoopa njokaluzi.
-Kumeneku ndi kuopa chinthu chosayenera kuopedwa.
Wani tambala ilibe chenje.
-Pabanja pamafunika kukhala mwamuna mmodzi ndi mkazi
mmodzi basi.
Wanjala safuna ndiwo.
-Munthu amene wayamba kuona kuti ndiwo zake sizikukoma
amakhala kuti wakhuta. Wanjala saona zonsezo amangoti bola
akhute.
Wanjala salima, amalima ngwokhuta.
-Kuti munthu agwire ntchito amafunika kudyera kaye.
Wanjiru sagonera, mvula yake ndi imodzi.
-Anthu oipa sakhalitsa.
Wanyanga aferanji?
-Mwambiwu umatanthauza kuti n’chifukwa chiyani munthu
wodalira mankhwala amafa? Aliyense adzafabe afune asafune.
Waona kamwana tola, ukulu n’kuona kako.
-Munthu akayenda ndi mwana amayenera kukhala wokonze-
kera. Si bwino kumangodalira mwanayo pa chilichonse.
Waona mawanga a Nkhanga wataya Nkhwali.
-Ukamamvera za anthu umatha kutaya mwayi womwe uli nawo
kale. Ukakhala ndi chinthu si bwino kuchinyoza chifukwa
waona china chokongola kwambiri kuopera kuti ungataye
chabwino n’kulephera kupeza chinacho.
Wapala moto kudambwe eni ake alipo.
-Mawuwa amatanthauza kuti wapalamula. Kapena kuyankhula
254