Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 254

Miyambi ya Patsokwe Wamtengatenga sagona. -Munthu akafuna kuchita chinthu amafunika kuchita khama m’malo mochita ulesi. Ngati anthu amene amanyamula zinthu samatopa kapena kugona. Wamuonetsa chidameta mduliro nyani. -Mawuwa amatanthauza kukhaulitsa munthu wina. Wamuonetsa chidameta nkhanga mpala -Mawuwa amatanthauza kukhaulitsa munthu wina. Wamusiya ali njo! pabwalo. -Mawuwa amanenedwa anthu akamaseka munthu yemwe pab- walo lamilandu amasowa chonena. Amayamba kumukuwiza n’kumauza amene akuoneka kuti tikuwayenderawo mawu ame- newa. Wamva m’mimba ndi amene amatsegula chitseko. -Munthu amene ali pamavuto ndi amene amachitapo kanthu kuti mavutowo amuchoke. Wandalama sayimba nthungululu. -Si bwino kumanyada ukakhala pabwino. Wandibisira mpeni kumphasa. -Mawuwa amanenedwa ngati munthu akudandaula kuti wina wawachitira chiwembu. Wandigwiritsa fuwa lamoto. -Mawuwa amanenedwa ndi munthu amene wapusitsidwa ndi winawake. Wandiviika m’mbuna. -Mawuwa amatanthauza kusungira munthu chakukhosi kuti udzamubwezere nayenso akadzalakwa. 253