Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 253
Miyambi ya Patsokwe
bwino. Si bwino kutengeka ndi zinthu chifukwa cha maon-
ekedwe. Ukhoza kupezeka kuti wataya mwayi wopezapeza.
Walira mvula walira matope.
-Chilichonse chili ndi zovuta zake, choncho si bwino kungosiya
kuchita zinthuzo chifukwa choti ukukumana ndi mavuto.
Tiyenera kumavomereza zotsatira za zomwe tasankha monga
kulowa m’banja.
Wamenya chikambakamba mtima uli pansi.
-Mawuwa amatanthauza kuti munthu walephera kuchita
zimene umafunadi kuchita.
Wamisala anaona nkhondo.
-Si bwino kunyoza munthu chifukwa santha kuchita zinthu zina
chifukwa ali ndi mbali ina yomwe amachita bwino. Osamanyoza
zonena za ena ngakhale kuti ndi ana kapena osaphunzira. Chifu-
kwa nthawi zina zimene anganene zimakhala zothandiza kwam-
biri.
Wam’kachisi amadya zam’kachisi.
-Munthu amapeza zimene akufunikira pamene amagwira ntchi-
to.
Wamkulu salakwa.
-Munthu wamkulu ngakhale alakwitse sauzidwira pagulu pom-
wepo kuti walakwa, koma kumukokera pambali.
Wampota bwanji khobwe ndili ku ula?
-Mkazi anapota khobwe kapena kuti kumupanga chipere, pom-
we mwamuna wake ankakonda wochita kubwira. Zimenezi zi-
nakhumudwitsa mwamunayo moti anakwiya. Chilichonse
chimakhala ndi dongosolo lake, choncho ndi bwino kumafunsa
tisanachite zinthu.
252