Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 251
Miyambi ya Patsokwe
n’kupita kwa wogulitsa n’kukapeza zitatha. Wogulitsayo an-
gamuuze kuti, “waimba yakale, ana aakazi abwerera.”
Waisenzera pankhongo.
-Amenewa ndi mawu okokomeza onena kuti nkhani sanaimvet-
se munthuyo.
Wakaduka alibe anansi.
-Munthu ukakhala wakaduka anthu amakuthawa.
Wakalamba Wafuna.
-Masiku ano anthu ambiri akumachita zinthu zomwe zingathan-
dize kuti asaoneke okalamba kwambiri, ndiye akamatchula
mwachining’a amangoti, “wakalamba wafuna.”
Wakhala kuutsi dala.
-Munthu akamafuna kuchoka amachita zinazake kuti achokepo.
Mwambiwu umaziyerekezera ndi kukhala dala kuutsi kuti uziti
wachoka chifukwa utsi ukukupwetseketsa maso.
Wakhalira khute.
-Mawuwa amatanthauza kudikirira zinthu zimene sitingazipeze.
Wakhate samunamiza nsapato.
-Tisamalonjeze zinthu zomwe sitingakwanitse kuchita, monga
kunamiza wakhate kuti umugulira nsapato. Komanso si bwino
kulonjeza munthu mphatso yomwe sangathe kuigwiritsa ntchi-
to. Umenewu umakhala mwano.
Wakhungu akakuuza kuti ndikugenda, samala, waponda
mwala!
-Munthu amene sumaganizira akakuuza zinazake zachilendo,
dziwa kuti palipo pamene akudalira.
Wakhungu akati ndikugenda, ndiye kuti waponda mwala.
-Munthu akamachita chinachake amakhala ndi podalira.
250