Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 250

Miyambi ya Patsokwe wachita zimene mwambiwu umanena, msamphawo umafwam- phuka n’kumuvwapula. Wagwa m’mbuna yosavundikira. -Mawuwa amatanthauza kuti munthuyo walakwa dala. Mbuna ndi dzanje limene anthu amatchera nyama n’kuima timaudzu pamwamba kuti nyamayo isazindikire kuti pali dzenje. Ndiye ngati munthu atagwa m’mbuna yosavundikira, ndiye kuti amaona kuti pali dzenje. Wagwira pa Mbira, Nungu ali ndi ngololo. -Mawuwa amanenedwa ngati munthu wataya chinachake kapena waluza ndalama moti zoti aipezanso aiwale. Waika phale watama mano. -Munthu amene amakazinga chimanga ndiye kuti ali ndi mano. Ndi bwino tizizindikira zinthu zimene tingathe kuchita kapena ayi. Waimba muluzi m’chimbudzi ndiye kuti anakhuta. -Munthu sungapite kuchimbudzi ulibe cholinga. Munthu amene amati akakhala pamavuto n’kumasangalala kapena kumaimba muluzi ndiye kuti akudziwa zoti mavuto akewo atha posachedwa kapena akuimba mlandu munthu wina. Waimba ng’oma yowambawamba. -Mawuwa amanenedwa ngati wina wachita zimene ena ama- yembekezera. Kapena ngati wachita zinthu zimene enanso ama- funa. Anthuwo akamanena amati, “Waimba ng’oma yowam- bawamba.” Waimba yakale, ana aakazi abwerera. -Mawuwa amanenedwa potanthauza kuti munthuyo wachedwa. Mwachitsanzo, munthu akhoza kumafuna kugula chinachake 249