Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 25
Miyambi ya Patsokwe
yangogwa. Komanso munthu amene wamwalira sangachite
chilichonse, ngati akuyankhula ndiye kuti adakali moyo.
Chakumbakumba chalema, chatenga mchira chayesa mala.
-Nthawi zina munthu amasiya kuyesayesa kuthetsa mavuto
n’kuyamba kumangokhala poganiza kuti atha okha.
Chakuti “tswo” chakuyambira, chakuti “tseche” chakupha.
-Tisamadandaule ndi zovuta zomwe zimabwera
pang’onopang’ono koma zomwe zimabwera kamodzim’ka-
modzi.
Chakwathu n’chakwathu adamangira nkhokwe m’nyumba.
-Ndi bwino kumamvera zimene ena akunena. Osamangoumirira
njira zakale popanda chifukwa chomveka bwino, chifukwa
mapeto ake timapezeka kuti talakwitsa.
Chala chimodzi sichiswa nsabwe.
-Palibe munthu amene angathe kuchita zonse payekha. Chon-
cho, ndi bwino kumadalirana. Pogwira ntchito kapena pothetsa
vuto, thandizo la anthu ena ndi lofunika.
Chala sicholoza mwini.
-Munthu sakonda kuona kulakwa kwake koma kwa ena.
Chalaka (chakanika) Bakha, Nkhuku singatole.
-Chimene chakanika katswiri munthu wamba sangachithe.
Chalaka Galu, fupa la matongwe.
-Mawu amenewa amanena za munthu yemwe ndi wosamva
ngakhale mutamulangiza motani. Amakhala ngati fupa louma
lomwe agalu alephera kuliswa.
Chalaka Nyani chili ndi khambi.
-Munthu akasiya chizolowezi chake ndiye kuti chilipo chimene
chamudabwitsa kapena chamuchititsa mantha.
24