Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 249

Miyambi ya Patsokwe Wadzoladzola matope, kumunda kulibe ndime. -Mawuwa amanena za munthu waulesi amene amayerekezera kuti walima koma asanalime, kungodzola matope kuti azioneka ngati amalima. Wafa atamva. -Mawuwa amanenedwa zikakhala kuti munthu wina wakumana ndi mavuto chifukwa chosamva. Wafa chona, khoswe akondwe. -Mawuwa amanenedwa anthu akamasangalala kuti munthu amene amavuta pamudzi wachoka, kapena wamwalira moti azikhalano mwamtendere. Wafa mphaka makoswe asangalale. -Mawuwa amanenedwa anthu akamasangalala kuti munthu amene amavuta pamudzi wachoka, kapena wamwalira moti azikhalano mwamtendere. Wafa ndi dama lake. -Pa Chichewa mawu akuti dama amatanthauza kunyada, anga- tanthauzenso kuchita chiwerewere. Ndiye mawuwa amatan- thauza kuti munthu wafa chifukwa cha kusamva kwake. Wafulumira kumeza asanatafune, ndiye cham’thimba pakhosi. -Tisamafulumire kuchita zinthu. Kuchita zinthu modekha n’ko- funika. Wafulumira kumeza kutafuna kukadakoma. -Tisamafulumire kuchita zinthu. Wagenda katauluka. -Kulephera kapena kunena mawu zinthu zitapita. Wakoka chingwe msampha uli pambuyo. -Mawuwa amanenedwa ngati munthu wapalamula chifukwa chosamvetsetsa kapena kusaonetsetsa bwino. Ngati munthu 248