Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 248
Miyambi ya Patsokwe
n’kumuchitira chipongwe balalo lisanapole. Tisamanyoze
kapena kuchitira chipongwe anthu amene akutithandiza.
Wachikumbakumba wasiya dzenje, kumudzi usakati “ndiwo!”
-Mawuwa amanena za munthu yemwe wapita kukafuna mbewa
ndiye wakumba n’kutopa n’kusiya una, ndiye kupita kunyumba
n’kumakadandaula kuti alibe ndiwo. Mwambiwu umagwiritsid-
wa ntchito ngati anthu akambirana zinazake ndiye akuuzana
kuti asakaulule zinthu zimene amakambiranazo.
Wachita mwa mlatho.
-Kuchita chinthu chinachake kuti upulumuke ngakhale kuti
sumafuna kuchichita.
Wachoka pa Chivuulandiwo wafika pa Chimwamchere.
-Mawuwa amanena za munthu amene anali woipa kale ndiye
waipiratu.
Wada m’mimba, akanakhala maso tikadatsukamo.
-Mwambi uwu umanenedwa zinthu zikavuta kwambiri moti
palibe chimene mungachite.
Wadabwa chule m’madzi muli mwake.
-Mawuwa amanenedwa ngati munthu wadabwa ndi zinazake
chifukwa choti si mmene zimayendera nthawi zonse.
Waduka lende, ana asewera pansi.
-Mawuwa amanenedwa ngati munthu wamwalira n’kusiya ana.
Wadula mchira.
-Mawuwa amanenedwa ngati munthu wina wapalamula kapena
wachita chinachake choipa. Mawu amenewa anachokera ku
zimene mchira wa buluzi umachita ukaduka.
Wadyera amakumba manda ake ndi mano.
-Dyera limaphetsa. Munthu akhoza kudwala matenda osiyana-
siyana chifukwa choti amadya kwambiri.
247