Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 245

Miyambi ya Patsokwe kumaganiza kaye ngati kuti, “Kodi mwini wake atandiuza kuti nditolele nthenga zomwe ndamwazazo, ndikwanitsadi kud- zitolera?” Usanayambe kudzitama kutalika, ndi bwino kumayamba waganizira kutalika kwa zinthu zimene zakuzungulira. -Mwambiwu umathanthauza kuti, kuti munthu ukhale wodzi- chepetsa, umafunika kumaganizira zimene anzako amachita bwino. Ndipo ukachita zimenezi mpamene umaona kuti anza- kowonso ndi ofunika. Usayimbe mbalule ukamachita bwino. -Mbalule ndi ng’oma. Ukaona kuti zikukuyendera si bwino ku- madzionetsera. Usiku ndi usiku ndithu, satungira mkanda. -Zochitika za usiku ndi zoopsa. Usiku kumakhala zilombo zo- opsa choncho ndi bwino kumachenjera poyenda usiku. Mwam- biwu ukutanthauza kuti sungaike timikanda pa ulusi usiku, kuli mdima. Choncho, chilichonse chili ndi nthawi yake yomwe un- gachichite. Usiku ndi usiku, ndithu udathawitsa Ligondo. -Zochitika za usiku ndi zoopsa. Usiku kumakhala zilombo zo- opsa. Choncho ndi bwino kumachenjera poyenda usiku. Usinini sungakule suposa dzino. -Dzino ndi lolimba kuposa usinini. Komanso mano ndi amene amaonekera pamwamba pa usininiwo. Si bwino kumadziona kuti ndife apamwamwa kwambiri kuposa ena omwe tawapeza kaya kuntchito kapena pamudzi. Utsi sufuka popanda moto. -Chilichonse chimakhala ndi chochititsa. Utsi sungafuke pamene palibe moto. 244