Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 244
Miyambi ya Patsokwe
Usamasule mtolo chifukwa muli liwiro la tonse.
-Munthu usanapute mlandu ndi bwino kumaganizira kuti zochi-
ta zakozo zikhudzanso anthu onse a m’banja lako.
Usamaswere dzungu m’lichero.
-Kuswera dzungu m’lichero kukungotanthauza kusaugwira mti-
ma. Ukamva nkhani yachilendo si bwino kuyamba kufotokozera
anthu chifukwa ukhoza kupezeka ukufalitsa mabodza.
Usamatame ntchito zake mtima wake usanaudziwe.
-Osamafulumira kuweruza munthu pa ntchito zake
usanamudziwe bwinobwino.
Usamathawe mkamwa, kumene ukupitakonso ukalipeza.
-Padziko lapansili anthu ambiri ndi am’kamwa moti palibe ku-
mene ungalowere osakapeza anthu otero.
Usamati ndathawa mlomo, kumene ukupitako ukaupeza.
-Kuthawa mlomo ndi kuthawa kulongolola. Mavuto ali
ponseponse ndipo sitingawathawe. Amene akufuna kuwathawa
kuli bwino angomwalira.
Usamati ndi chilonda, lidzakula.
-Mwana akalakwitsa ndi bwino kumulangiza m’malo mongo-
mulekerera. Kuti mwana akule bwino tiyenera kuyamba kumu-
langiza ali wamng’ono. Apo ayi chilonda chidzasanduka bala
lalikulu khalidwe lake litafika poipa.
Usanalavule mawu, yamba wawalawa kaye.
-Ndi bwino kumaonetsetsa kuti zimene tikunena ndi zoona ko-
manso zabwino, zomwe sizingakhumudwitse ena.
Usanamwaze nthenga, kumayamba waona kaye ngati un-
gazitolele.
-Kunena mabodza kuli ngati kumwaza nthenga. Nthenga zim-
apita ndi mphepo. Ndiye usananene bodza ndi bwino
243