Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 243
Miyambi ya Patsokwe
Usakhulupirire mazira a Koka.
-Mbalame ya Koka imafuna malo omwe Khwangwala waikira
kale mazira ake n’kumuthamangitsa kuti aikirepo ake. Choncho,
munthu sangadziwe dzira lomwe litulutse ana a Koka kapena a
Khwangwala. Mwambiwu umatanthauza kuti zam’tsongolo siz-
idziwika.
Usakonde vembe, koma ukonde chulu.
-Ukakwatira umakhala wakwatira mudzi wonse. Usamangokon-
da mkazi wako yekhayo komanso makolo ake.
Usalimbitse goli pomanga bulu wako.
-Pofufuza zinazake timafunika anthu kuwatenga
pang’onopang’ono kuti asachite mantha koma akhale omasuka.
Usamadikire kuti madzi afike m’nkhosi.
-Usamadikire kuti vuto liipe kwambiri ndiye n’kumayamba ku-
chitapo kanthu.
Usamakokomeze chisanu ngati chitolankhuni.
-Munthu akasauka asamangodandaula, koma azigwira ntchito
kuti umphawiwo umuchoke.
Usamaloze chitsa usanachibzole.
-Osamachenjeza anzako kapena kuwauza kuti asiye kuchita
zoipa zinazake zomwe iwenso umachita.
Usamanyoze thewera mkuzi uli nawo.
-Usamanyoze mkamwini wako pamene mwana wako adakali
nayebe.
Usamapake mnzako chipwidza.
-Mawuwa amanenedwa pouza munthu kuti asamanamizire
mnzake. Chipwidza ndi ndowe kapena matudzi a chiweto.
242