Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 242
Miyambi ya Patsokwe
Umavomera ngati womva (wodwala) dzino.
-Mawuwa amatanthauza kuvomera mokaikira, moti wina san-
gagwire chenicheni. Munthu amafunika kunena motsimikiza
osati mokayikira.
Umayambira madzi akadali m’mapazi.
-Vuto likamayamba kumene limakhala losavuta kuthana nalo
monga matenda, njala ndi zina.
Umayambirira madzi asanafike m’maondo.
-Vuto likamayamba kumene limakhala losavuta kuthana nalo
monga matenda, njala ndi zina.
Umayambiza madzi ali m’maondo.
-Vuto likamayamba kumene limakhala losavuta kuthana nalo
monga matenda, njala ndi zina.
Umazika mzimbi woyera kumene wachoka ndi kumene upita.
-Kulikonse kumene wachoka ndi kumene ukupita ndi bwino
kusiya mbiri yabwino kuti anthu adzakulandirenso mawa.
Mzimbi yoyera ndi nthenga yoyera, yomwe ikuimira mbiri
yabwino.
Umphawi n’kulumpha chiunda.
-Munthu ukachoka kwanu umasowa zambiri zimene unkazipe-
za kwanu. Anthu amavutika akakhala koyenda.
Unjiunji ajiwitsa.
-Kukondetsa zinthu kumabweretsa mavuto makamaka zinthuzo
zikakhala zoipa.
Unyinji ukoma, uipira kutha mchere.
-Kuchulukana n’kwabwino, kumangoipira kuti zinthu siz-
ichedwa kutha. Koma pakakhala ntchito imayenda ndithu.
241