Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 240
Miyambi ya Patsokwe
unamuuza kuti, “Musachite mantha achimwene. Panotu ta-
kumana amuna okhaokha. Kaya inu mukuchokera kuti ulen-
dowu?” Poyankha munthu uja anati: “Ine ndikuchokera
m’malunjemu ndimakasaka.” Ndiyeno mkango unati, “Popeza
tonse tikuchokera kosaka, aliyense asaulule mnzake. Ulenje
umasimba wako, osati wamnzako.” Atangosiyana pamenepo,
mkango uja unalowa m’tchire ndipo munthuyo anathamangira
kwawo ali ndi mantha. Kenako anayamba kuuza anthu kuti wa-
kumana ndi mkango utagwira nyama. Mkango uja utamva zim-
enezi, unapita kunyumba kwa amfumu n’kukagwira mwana
wawo n’kumupha. Kenako unakamuika m’nyumba mwa mlenje
uja. M’mudzimo munayambika chipwirikiti chifukwa cha
kusowa kwa mwanayo ndipo mfumu inalamula kuti anthu
afufuze amene watenga mwana wakeyo. Atafufuza anapeza
mwanayo atafa koma ali m’nyumba mwa mlenje uja ndipo mfu-
mu inalamula kuti nayenso aphedwe.
Ulesi ndi matenda.
-Ukalekerera ulesi chimakhala chizolowezi ndipo chimasanduka
matenda.
Ulesi ulibe mtolo.
-Ulesi umabweretsa njala komanso mavuto ena. Munthu waulesi
sangakhale ndi kanthu kolozeka.
Ulumbwana ulibe mainja awiri.
-Mawuwa amatanthauza kuti munthu sangakhale mwana
n’kupezeka kuti wakhalapo mudzi wina n’kusamuka, kenako
n’kubwereranso kubwinja loyamba lija. Mwambiwu umatan-
thauza kuti munthu akamakula amafunika kusiya chibwana.
Munthu akakhala mwana nthawi zambiri sachita zinthu
mozindikira.
239