Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 24
Miyambi ya Patsokwe
n’kuyamba kumuchitira zoipa. Ndi bwino kumangoyamikira
chifukwa sudziwa chidzachitike mawa. Mwina mwayi udzakha-
la wako.
Chakubala chimasanzitsa, obereka amanyansidwa.
-Makolo ayenera kukhutira ndi mphatso za ana omwe Mulungu
wawapatsa.
Chakudya chawekha sichikoma, koma cholimbirana.
-Pali zinthu zina zomwe sizikoma kupanga wekha monga map-
wando, ntchito komanso zina. Ndi bwino kumagawanako ndi
ena zimene tili nazo.
Chakudya chimodzimodzi sichinona.
-Ndi bwino kumasinthasinthako pochita zinthu.
Chakudya chimodzimodzi sichinonetsa.
-Si nzeru munthu kukhulupirira nzeru zake zokha. Ndi bwino
kumafunsako ena kuti tikhale ndi chinthunzithunzi chokwanira
cha moyo kapena ntchito.
Chakudya sichichepa, chimachepa ndi chovala.
-Chovala chimodzi simungathe kuvala anthu awiri nthawi
imodzi. Koma chakudya ngakhale chitachepa bwanji mukhoza
kugawana. Mawuwa amanenedwa poitanira ena kuti adzadye
nawo chakudya. Kumayamikira zimene timapeza.
Chakudza sichiimba ng’oma.
-Kumakonzekera zam’tsogolo, chifukwa zamawa sizidziwika.
Chakufa sichiopa kutulutsa fungo.
-Chilichonse chimakhala ndi zotsatira zake ndipo sitingaziletse.
Munthu amene walakwa walakwa basi. Mbiri yake imaipa ndipo
amapatsidwa chilango.
Chakufa sichiyankhula.
-Munthu amene kunalibe sangaikire umboni pa nkhani imene
23