Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 239

Miyambi ya Patsokwe Ulemu wa Nkhukhu wopalasa pali anthu. -Mwambiwu umanena za munthu wopanda ulemu. Ulendo n’kaphatikira, ukalinda wako wachedwa. -Mawuwa amatanthauza kuti ukamapita kwinakwake uma- yenera kupita ndi anzako, ukadikira ulendo wako umachedwa. Kuyenda ndi anzako kumathandiza, ukakhala wekha sungakwanitse kuchita zinthu zina. Ulendo n’kudyera. -Kuti munthu uyende ulendo makamaka ngati ndi wapansi, umafunika kudyera. Kudya kumatipatsa mphamvu zoti tigwire ntchito. Ulendo ndi uwu wachoka. -Kuchita chinthu kumafuna kuchiyamba osati kumangoyank- hula. Ulendo wa awa wakutha kamba. -Kamba ndi chakudya cha paulendo. Kuchedwetsa zinthu ku- mawonongetsa zambiri kapena kubweretsa chipwirikiti. Ulesi ndi mphwayi zimayambitsa umphawi. Ulendo wa awa wakutha nkhokwe. -Kuchedwetsa zinthu kumawonongetsa zambiri kapena kubwer- etsa chipwirikiti. Ulesi ndi mphwayi zimayambitsa umphawi. Ulenje umasimba wako. -Osamakonda kunena za ena, ukhoza kupalamula. Nkhani yake imanena kuti, kalekale panali munthu wina amene anapita kuthengo kukapha nyama. Kumeneko anapha nyama ziwiri. Pamene ankabwerera kwawo n’kuti kunja kuli kachisisira ndipo anamva phokoso likumveka m’mudzi wakwawo. Atafika pam- phambano, mwadzidzidzi anangoona mkango watulukira. Mlenjeyo anachita mantha kwambiri, koma mkango uja 238