Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 235
Miyambi ya Patsokwe
anapezako anzake amene anali atakhala kwa nthawi yaitali ndi
bwanayo. Anzakewo anali ndi zinthu zambiri zimene anapata
pa zaka zimene anakhala akugwira ntchito. Chifukwa chosirira
kukhala ndi katundu ngati wa anzakeyo ndiponso kukhala
wolemera, anaganiza zoti apeze mankhwala. Mumtima anagani-
za kuti mankhwalawo amuthandiza kuti bwana wake azi-
mukonda, kuti iye akhupuke ndiponso kuti bwanayo achotse
ena mwa anzake ena amene sankagwirizana nawo. Ngati zime-
nezi zikanatheka ndiye kuti iye akanalandira udindo ndiponso
akanamuwonjera malipiro ake. Atapita kwa sing’anga anapezadi
mankhwala amene ankafunawo. Sing’anga uja popereka
mankhwalawo anamuuzitsa kuti asakagone kwa masiku atatu
chifukwa ngati angakagone ndiye kuti akatupa mimba. Koma
tulo ndi nkhondo timagoneka olira. Tsiku loyamba analimbadi
m’maso osagona. Pamene kunkacha tsiku lachiwiri tulo tinali ti-
tasonkhana, moti amati akati aimirire sizimatheka. Atakhala
pansi kuyambika kwa matenda kunali komweko. Anzake amene
ankafuna kuwalodza aja atamufunsa anafokotokoza kuti,
“Pepani anzanga, munthune ndimafuna kulemera. Ndiye
mankhwala amene ndinapeza, chizimba chake china n’choti
ndisagone masiku atatu, koma ndalephera kuchikwaniritsa.
Motero thamangani mukamuuze sing’anga wandipatsa
mankhwalawa kuti atsukule nyangayo n’cholinga choti ine
ndikhale ndi moyo.” Anzake aja atapita anakapeza kuti
sing’anga uja anali atamwalira cha dzana lake moti anthu anali
asanachoke pasiwa. Anzake atabwerako anamufotokozera
mmene ayendera. Chifukwa chodziwa kuti kwake kwatha
anayamba kulira ndipo polirapo anali kulira mochenjeza kuti,
“Abale anga munthu ukasauka si nzeru kugwira nyanga,
taonani zandichitikira inezi!” Pamenepo anzakewo anavo-
merezadi kuti, “Ukasauka usamagwire nyanga.” Nyanga
234