Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 234
Miyambi ya Patsokwe
Ukapha tonde wonona, usamathe mawu.
-Tisamanyade kapena kudzitama tikakhala ndi chinthu
chinachake.
Ukapindula wotcha, akazi ndi alendo.
-Munthu asamaiwale kapena kunyoza abale ake chifukwa cha
mkazi, banja limatha koma chibale sichitha.
Ukapita kuthengo usamakhudzane ndi mtuvituvi, ungawonje-
zere kununkha.
-Osamaloza ena chala chifukwa cha zolakwa zako. Anthu ena
akalakwa amayamba kuloza ena zala kuti ndiye alakwitsa
kapena achititsa kuti alakwe.
Ukaponya chakudya pamadzi, udzachipeza.
-Ndi bwino kukhala woolowa manja chifukwa tsiku lina anthu
omwe ukuwathandizawo angadzakugwire dzanja.
Ukasauka usadzimangilire.
-Munthu ukasauka usamadzichitire zoipa, monga kudzikhweza
kapena kumwa tameki, chifukwa palibe chomwe ungapindu-
lepo.
Ukasauka usamagwire nyanga.
-Ngati ndife osauka tizivomereza m’malo moyamba kudalira
nyanga, kuba kapena kupha anthu.
Ukasauka usamaloze anzako chala.
-Ukasauka usamanamizire anzako kuti ndiye akupangitsa.
Ukasawuka usamagwire nyanga.
-Si bwino kumachitira ena nsanje kapena kumawafunira zoipa
ukakhala kuti iweyo ulibe kapena sungathe kuchita zinazake.
Nkhani yake imati, mkulu wina anakafunsira ntchito kwa bwa-
na wolemera kwambiri. Kumene ankagwira ntchitoko
233