Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 233

Miyambi ya Patsokwe nsima yake. Ukapalamula uzikhala wokonzeka. -Munthu ukalakwa umayenera kuyembekezera kuti ukumana ndi zotsatirapo zake. Ukapalana ubwenzi ndi mphezi, suopa kung’anima. -Munthu amene akufunitsitsa chinthu ayenera kukhala wolimba mtima. Ukapalana ubwenzi ndi Vumbwe umakhala uli ndi Nkhuku. -Tizikhala titakonzeka tisanayambe kuchita chilichonse. Kuti an- thu azikonda kubwera pakhomo umafunika kumawadyetsa bwino. Ukapeza ana a olemera akukazinga maso a nkhono, kazinga nawo. -Tizichita zimene anzathu akuchita. Ukapeza anzako akukazinga maso, nawenso kazinga ako. -Munthu uzichita nawo zomwe eni mudzi akuchita kapena wa- wapeza akuchita. Ukapeza anzako akutong’ola maso, nawe tong’ola ako. -Tizichita zimene anzathu akuchita. Ukapeza eni mudzi akukazinga maso, nawenso kazinga ako. -Tizichita zimene anzathu akuchita. Ukapeza nyamu zikuuluka, ima pambali uzitola imodziimodzi, upeza zadzaza nsengwa. Koma ukaikapo dzan- ja, udzatola imodzi yokha. -Munthu ayenera kumachita zinthu mofatsa kuti apeza zabwino. Dyera komanso changu nthawi zina sizithandiza. Ukapha mwiri umabweza mphanda. -Munthu akalemera amakhala wokongola ngati mwiri. Ndiye zikatero si bwino kuyamba kunyada n’kumanyoza ena. 232