Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 231
Miyambi ya Patsokwe
Ukakwera m’mwamba usamatukwane pansi, ungasowe woku-
tola ukatsakamuka.
-Si bwino kumanyoza ena ukakhala pabwino chifukwa zik-
adzakuvuta udzasowa wokuthandiza.
Ukakwera m’mwamba usamatukwane pansi.
-Ukakhala pabwino usamanyoze anzako chifukwa zikadzakuvu-
ta udzasowa wokuthandiza. Mwachitsanzo, ukamatukwana an-
thu omwe ali pansi ukakwera mumtengo, ukatsakamuka
umasowa wokutola.
Ukakwera pamsana pa njovu, usamati kulibe mame.
-Osamachita matama ukakhala pabwino chifukwa za mawa siz-
idziwika. Ukakhala pabwino usamanyoze anzako.
Ukalakwa usamafulumire kupita kuboma.
-Kumayamba watsikiza kuti ndiwe wosalakwa ukamapita ndi
nkhani kuboma chifukwa ukhoza kungomangidwa nazo ulele.
Ukalemera cheuka, ona chakulemeretsa.
-Tisamaiwale anthu amene atithandiza kuti tifike pano.
Ukalemera tsekako, ‘kulinji’ akudza m’njira.
-Ukalemera usamadzitame chifukwa akuba akhoza kukubera
iwe n’kufota. Chakudza sichiimba ng’oma.
Ukalemera umayankhulira m’chigulu.
-Tikalemera tisamaonetse zonse zomwe tili nazo chifukwa ena
akhoza kutibera. Chigulu ndi chikho chomwera mowa. Kuyank-
hulira m’chigulu kukusonyeza kuti suima pachulu n’ku-
mabwebwetuka za kulemera kwako.
Ukalemera usamavinire poyera, koma m’nyumba.
-Tikalemera tisamaonetse zonse zomwe tili nazo, chifukwa ena
akhoza kutibera.
230